Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • lmd 3
  • Kukoma Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukoma Mtima
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Yesu Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
  • Kuchita Chidwi ndi Anthu
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kukhala Achifundo
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kukambirana Mwachibadwa
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kodi Yesu Ali Ndi Makhalidwe Otani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd 3

ULENDO WOYAMBA

Yesu mokoma mtima akukhudza munthu wavuto losaona kuti amuchiritse.

Yohane 9:1-7

PHUNZIRO 3

Kukoma Mtima

Mfundo yaikulu: “Chikondi . . . n’chokoma mtima.”​—1 Akor. 13:4.

Zomwe Yesu Anachita

Yesu mokoma mtima akukhudza munthu wavuto losaona kuti amuchiritse.

VIDIYO: Yesu Anachiritsa Munthu Wavuto Losaona

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Yohane 9:1-7. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi Yesu anayamba n’kutani, kuchiritsa munthuyo kapena kukambirana naye uthenga wabwino?​—Onani Yohane 9:35-38.

  2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mmene Yesu anafikira, zinathandiza kuti munthuyo amvetsere uthenga wabwino?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Nthawi zambiri munthu angachite chidwi ndi uthenga wathu akaona kuti tikuchita naye zinthu momuganizira.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzikhala achifundo. Muziganizira mmene munthuyo akumvera.

  1. Dzifunseni kuti: ‘Kodi akhoza kukhala kuti akuda nkhawa ndi chiyani? Kodi angasangalale nditamuuza zotani?’ Mukamaganizira zimenezi, mwachibadwa mudzamusonyeza kukoma mtima.

  2. Muzisonyeza kuti mukumudera nkhawa pomumvetsera. Akakuuzani mmene akumvera ndi nkhani inayake kapena akakuuzani mavuto omwe akukumana nawo, musamasinthe nkhani.

4. Muzilankhula mokoma mtima komanso mwaulemu. Ngati mwakhudzika ndi munthuyo ndipo mukufunitsitsa kumuthandiza, adzazindikira zimenezo poona mmene mukulankhulira. Muzisamala ndi zomwe mukulankhula komanso mmene mukulankhulira kuti musamukhumudwitse.

5. Muzikhala ofunitsitsa kuthandiza. Yesetsani kupeza mipata yothandizira munthuyo. Mukamachita zinthu mokoma mtima simudzavutika kuyamba kukambirana ndi anthu.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma 12:15, 16; Agal. 6:10; Aheb. 13:16

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani