Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • lmd 4
  • Kudzichepetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudzichepetsa
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Paulo Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo
  • Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Musamadziganizire Kuposa Mmene Muyenera Kudziganizira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Kulankhula Mwaluso
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd 4

ULENDO WOYAMBA

Mtumwi Paulo wamangidwa unyolo limodzi ndi msilikali womulondera. Iye akulankhula mwaulemu kwa Mfumu Agiripa, Bwanamkubwa Fesito ndi Berenike.

Machitidwe 26:2, 3

PHUNZIRO 4

Kudzichepetsa

Mfundo yaikulu: “Modzichepetsa, muziona kuti ena amakuposani.”​—Afil. 2:3.

Zomwe Paulo Anachita

Mtumwi Paulo wamangidwa unyolo limodzi ndi msilikali womulondera. Iye akulankhula mwaulemu kwa Mfumu Agiripa, Bwanamkubwa Fesito ndi Berenike.

VIDIYO: Paulo Analalikira Mfumu Agiripa

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Machitidwe 26:2, 3. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kudzichepetsa pomwe ankalankhula ndi Mfumu Agiripa?

  2. Kodi Paulo anatani kuti anthu aziganizira kwambiri za Yehova komanso Malemba m’malo moganizira za iyeyo?​—Onani Machitidwe 26:22.

Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo

2. Anthu amachita chidwi ndi uthenga wathu tikakhala odzichepetsa ndi aulemu.

Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo

3. Muzilankhula mwaulemu. Pewani kudzionetsera ngati wodziwa chilichonse komanso ngati kuti winayo palibe chomwe akudziwa. Muzilankhula naye mwaulemu.

4. Muzisonyeza kuti uthenga wanu ukuchokera m’Baibulo. Mawu a Mulungu ali ndi mfundo zomwe zimafika anthu pa mtima. Tikamawagwiritsa ntchito, timathandiza anthu kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.

5. Muzikhala odekha. Musamakakamire kuonetsa kuti mfundo yanu ndi imene ili yolondola. Sitifunikira kumakangana ndi anthu. Muzisonyeza kudzichepetsa pokhala odekha komanso kuchokapo zinthu zisanafike poipa. (Miy. 17:14; Tito 3:2) Mukakhala odekha mutha kudzalankhulanso ndi munthuyo nthawi ina.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma 12:16-18; 1 Akor. 8:1; 2 Akor. 3:5

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani