NYIMBO 139
Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano
- 1. Yerekeza ukuona; - Iwe ndi ’ne m’dziko latsopano. - Ona mmene udzamvere - Kukhala m’dziko lamtendere. - Oipa onse achoka. - M’lungu wathu sadzalephera. - Kusintha zonse padziko lapansi, - Tidzamuimbira nyimbo - tikumati: - (KOLASI) - “Tikuthokoza mwachita bwino. - Zonse zakhaladi zatsopano. - Tikuimba nyimbo mwachisangalalo - Ndinudi woyenera ulemerero.” 
- 2. Taganizira m’tsogolo; - Iwe ndi ’ne m’dziko latsopano. - Sitidzamva ndi kuona - Zinthu zotichititsa mantha. - Mmene analonjezera; - Zinthu zonse zachitikadi. - Tsopano aku’kitsanso akufa; - Iwo ndi ife - tidzamuyamikira: - (KOLASI) - “Tikuthokoza mwachita bwino. - Zonse zakhaladi zatsopano. - Tikuimba nyimbo mwachisangalalo - Ndinudi woyenera ulemerero.” 
(Onaninso Sal. 37:10, 11; Yes. 65:17; Yoh. 5:28; 2 Pet. 3:13.)