NYIMBO 24
Bwerani Kuphiri la Yehova
zosindikizidwa
	- 1. Phiri la Yehova, - Tangoliyang’anani. - Latalika kuposa - Ena onse lero. - Anthu akubwera, - Kuchokera kutali, - Akuitanizana, - ‘Bwerani kwa M’lungu.’ - Tsopano wamng’ono - Wakhala mtundu waukulu, - Tikuona kuti, - Tikudalitsidwa ndi M’lungu. - Ambiri tsopano - Akuvomerezadi. - Ulamuliro wake - Mokhulupirika. 
- 2. Yesu walamula - Kuti tipite ndithu. - Tikalalikire - Uthenga wa Ufumu. - Khristu wayambano - Ulamuliro wake. - Iye akuti tikhale - Kumbali yake. - Ndi zosangalatsa, - Kuona khamu lalikulu. - Likukulirabe, - Ndipo tonse tikuthandiza. - Tonse tifuule, - Tiitanetu anthu, - ‘Bwerani kuphiri - la Yehova Mulungu.’ 
(Onaninso Sal. 43:3; 99:9; Yes. 60:22; Mac. 16:5.)