NYIMBO 150
Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke
zosindikizidwa
	- 1. Mitundu ya anthu - Ikutsutsabe Yesu. - Ulamuliro wa anthu - Utha watero M’lungu. - Ufumu wa M’lungu - Ukulamuliradi. - Yesu adzachotsa adani. - Adzatha posachedwa. - (KOLASI) - Bweranitu kwa Yehova - Kuti mudzapulumuke. - Musakayike, - Muzimumvera, - Mukhale kumbali yake. - Adzakupulumutsani - Ndi mphamvu zake. 
- 2. Anthu akusankha - Kumvetsera uthenga. - Timalalikira onse. - Enatu amakana. - Tikamavutika - Tisakhale ndi mantha. - M’lungu adzatisamalira - Timukhulupirire. - (KOLASI) - Bweranitu kwa Yehova - Kuti mudzapulumuke. - Musakayike, - Muzimumvera, - Mukhale kumbali yake. - Adzakupulumutsani - Ndi mphamvu zake. 
(Onaninso 1 Sam. 2:9; Sal. 2:2, 3, 9; Miy. 2:8; Mat. 6:33.)