NYIMBO 89
Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso
zosindikizidwa
1. Kodi timamveradi Yesu Khristu
Pa zonse zimene ananena?
Zomwe anaphunzitsa ndi zabwino.
Tidalitsidwa tikazimvera.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze,
Mvera udalitsidwe.
2. Monga nyumba yomangidwa pathanthwe
Osati yomangidwa pamchenga.
Zochita zathu zingatiteteze,
Kokha ngati Yesu timumvera.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze,
Mvera udalitsidwe.
3. Monga mtengo wamumbali mwa madzi
Umabereka nthawi ’kafika,
Tikamvera tidzadalitsidwadi,
Moyo wosatha tidzalandira.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze,
Mvera udalitsidwe.
(Onaninso Deut. 28:2; Sal. 1:3; Miy. 10:22; Mat. 7:24-27; Luka 6:47-49.)