NYIMBO 126
Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu
zosindikizidwa
1. Khala maso, upirire,
Ukhalebe wamphamvu.
Ukhale wolimba mtima,
Udzapambana ndithu.
Timvera lamulo la Yesu;
Tikhalebe kumbali yake.
(KOLASI)
Khala maso, khala wamphamvu!
Limba mpaka mapeto!
2. Khala maso, usagone,
Wokonzeka kumvera.
Uzimvera malangizo
Ochokera kwa Yesu.
Mvera malangizo a ’kulu,
Oteteza nkhosa, n’cho’nadi.
(KOLASI)
Khala maso, khala wamphamvu!
Limba mpaka mapeto!
3. Khala maso, m’gwirizane
Poteteza uthenga.
Ngakhale uzitsutsidwa,
Uzilalikirabe.
Tamanda M’lungu mwachimwemwe.
Tsiku lake layandikira!
(KOLASI)
Khala maso, khala wamphamvu!
Limba mpaka mapeto!
(Onaninso Mat. 24:13; Aheb. 13:7, 17; 1 Pet. 5:8.)