NYIMBO 88
Ndidziwitseni Njira Zanu
zosindikizidwa
1. Yehova tasonkhanatu pamodzi,
Pomvera kuitana kwanu.
Mawu anu ndi nyale m’njira yathu,
Amatiphunzitsa za inu.
(KOLASI)
Ndiphunzitseni njira zanuzo;
Ndikhale womvera malamulo.
Ndiyendetseni m’njira yoona,
Malamulo anu ndizikonda.
2. Nzeru zanu Yehova ndi zakuya,
Mfundo zanu n’zolimbikitsa.
Mawu anu adzakhala kosatha,
Timapezamo zodabwitsa.
(KOLASI)
Ndiphunzitseni njira zanuzo;
Ndikhale womvera malamulo.
Ndiyendetseni m’njira yoona,
Malamulo anu ndizikonda.