NYIMBO 130
Muzikhululuka
zosindikizidwa
1. Mwachikondi M’lungu
Anapereka Yesu
Kuti tikhululukidwe,
Ndi kuthetsanso imfa.
M’lungu amakhululuka,
Ngati ife talapa.
Nsembe ya dipo ya Yesu,
Imatithandizadi.
2. Tikamatsanzira
Chifundo cha Yehova
Pokhululukira ena,
Tidzakhululukidwa.
Tikhale ololerana,
Ndipo tisamadane;
Tizilemekeza ena,
Komanso kuwakonda.
3. Chifundo n’chabwino
Tonse tikhale nacho.
Sitidzasunga zifukwa,
Tikakhumudwitsidwa.
Tikatsanzira Yehova,
Yemwe ndi wachikondi,
Tidzakhululukirana;
Tidzafanana naye.
(Onaninso Mat. 6:12; Aef. 4:32; Akol. 3:13.)