NYIMBO 76
Kodi Mumamva Bwanji?
- 1. Kodi m’mamva bwanji - Mukasonyeza khama - Polalikira anthu - Ndi kuwaphunzitsa? - Mukamayesetsa - M’lungu adzadalitsa. - Mudzathandiza anthu - Kudziwa Mulungu. - (KOLASI) - Timasangalala ndithu - Kupereka mtima wathu, - Choncho timutumikire - Tsiku lililonse. 
- 2. Kodi m’mamva bwanji - Mukadziwatu kuti - Mwawafika pamtima - Akamva uthenga? - Ena amakana, - Ena amatitsutsa. - Koma timanyadira - Tikalalikira. - (KOLASI) - Timasangalala ndithu - Kupereka mtima wathu, - Choncho timutumikire - Tsiku lililonse. 
- 3. Kodi m’mamva bwanji - Pokumbukira kuti - Mwa chikondi Yehova - Amatsogolera? - Timalalikira, - Timaphunzitsa anthu - Akhale ndi tsogolo, - Adzapeze moyo. - (KOLASI) - Timasangalala ndithu - Kupereka mtima wathu, - Choncho timutumikire - Tsiku lililonse. 
(Onaninso Mac. 13:48; 1 Ates. 2:4; 1 Tim. 1:11.)