B15
Kalendala ya Chiheberi KUSIYANASIYANA KWA NYENGO
| NISANI (ABIBU) March—April | 14 Pasika 15-21 Mkate Wopanda Zofufumitsa 16 Nsembe ya zipatso zoyamba kucha | Yorodano ankasefukira chifukwa cha mvula ndi madzi osungunuka | Balere | 
| IYARA (ZIVI) April—May | 14 Pasika Wochitika Nthawi Yake Itadutsa | Nthawi ya chilimwe, kumwamba kopanda mitambo | Tirigu | 
| SIVANI May—June | 6 Chikondwerero cha Masabata (Pentekosite) | Kunja kunkatentha koma kunkakhala mpweya wabwino | Tirigu, nkhuyu zoyambirira | 
| TAMUZI June—July | Kutentha kunkawonjezereka, mame ankagwa ambiri | Mphesa zoyambirira | |
| ABI July—August | Kutentha kunkafika pachimake | Zipatso zamʼchilimwe | |
| ELULI August—September | Kutentha kunkapitirira | Kanjedza, mphesa ndi nkhuyu | |
| TISHIRI (ETANIMU) September—October | 1 Tsiku loliza lipenga 10 Mwambo Wophimba Machimo 15-21 Chikondwerero cha Misasa 22 Msonkhano wapadera | Chilimwe chikutha, mvula ikuyamba | Kulima | 
| HESHIVANI (BULI) October—November | Mvula yowaza— | Maolivi | |
| KISILEVI November—December | 25 Chikondwerero cha Kupereka Kachisi wa Mulungu | Mvula inkawonjezereka, madzi ankaundana mʼmapiri | Nyengo yozizira ziweto zinkakhala mʼkhola | 
| TEBETI December—January | Kunkazizira kwambiri, kunkagwa mvula, madzi ankaundana mʼmapiri | Zomera zikukula | |
| SEBATI January—February | Kuzizira kunkacheperako, mvula inkapitiriza kugwa | Amondi ankachita maluwa | |
| ADARA February—March | 14, 15 Purimu | Kunkachitika mabingu, kunkagwa mvula yamatalala | Fulakesi | 
| VEADARA March | Pa zaka 19 zilizonse, zaka 7 zinkakhala ndi mwezi wowonjezera |