Genesis
15 Ndiyeno zimenezi zitachitika, Yehova analankhula ndi Abulamu m’masomphenya,+ kuti: “Usaope+ Abulamu. Ine ndine chishango chako.+ Mphoto yako idzakhala yaikulu kwambiri.”+ 2 Abulamu atamva zimenezi anati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mudzandipatsa chiyani ine? Taonani ndilibe mwana ndipo amene adzakhale wolowa nyumba yanga ndi munthu wa ku Damasiko, Eliezere.”+ 3 Ananenanso kuti: “Simunandipatse mbewu+ ndipo mtumiki wanga+ ndiye adzakhale wolowa nyumba yanga.” 4 Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Munthu ameneyu sadzakhala wolowa nyumba yako ayi, koma munthu amene adzatuluke mwa iwe ndi amene adzakhale wolowa nyumba yako.”+
5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+ 6 Pamenepo iye anakhulupirira mwa Yehova,+ ndipo Mulunguyo anamuona Abulamu ngati wolungama.+ 7 Anamuuzanso kuti: “Ine ndine Yehova, amene ndinakuchotsa ku Uri wa kwa Akasidi, kudzakupatsa dzikoli kuti likhale lako.”+ 8 Ndipo iye anayankha kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, nditsimikiza ndi chiyani kuti dzikoli ndidzalitengadi kukhala langa?”+ 9 Pamenepo iye anauza Abulamu kuti: “Unditengere ng’ombe ya zaka zitatu yomwe sinaberekepo, mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, nkhosa yamphongo ya zaka zitatu, ndiponso njiwa yaing’ono ndi mwana wa nkhunda.”+ 10 Choncho iye anatenga zonsezi n’kuzidula pakati n’kuika mbali imodzi moyang’anana ndi inzake, koma mbalamezo sanazidule.+ 11 Ndipo mbalame zodya nyama zinayamba kutera pa nyama zophedwazo.+ Koma Abulamu anali kuziingitsa.
12 Patapita nthawi, dzuwa lili pafupi kulowa, Abulamu anagona tulo tofa nato.+ Pamenepo mdima woopsa wandiweyani unayamba kufika pa iye. 13 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti: “Udziwe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni,+ ndipo idzatumikira eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.+ 14 Koma mtundu umene adzautumikirewo ndidzauweruza.+ Pambuyo pake, iwo adzachokako ndi katundu wochuluka.+ 15 Kunena za iweyo, udzatsikira kwa makolo ako mu mtendere. Udzaikidwa m’manda uli wokalamba, utakhala ndi moyo wabwino ndi wautali.+ 16 Koma m’badwo wachinayi udzabwerera kuno,+ chifukwa nthawi yoti Aamori alangidwe sinakwane.”+
17 Tsopano dzuwa linali kulowa, ndipo kunayamba kugwa chimdima. Pamenepo, ng’anjo yofuka ndiponso muuni wamoto zinadutsa pakati pa nyama zodulidwazo.+ 18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu,+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+ 19 Ndidzapereka kwa mbewu yako dziko la Akeni,+ Akenizi, Akadimoni, 20 Ahiti,+ Aperezi,+ Arefai,+ 21 Aamori, Akanani, Agirigasi ndi la Ayebusi.”+