JULY 28–AUGUST 3
MIYAMBO 24
Nyimbo Na. 38 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzikonzekera Mavuto
(10 min.)
Muziphunzira Baibulo kuti mupeze nzeru zokuthandizani kudziwa zinthu (Miy 24:5; it-2 610 ¶8)
Musamasiye kuchita zinthu zokhudza kulambira ngakhale pamene mwafooka (Miy 24:10; w09 12/15 18 ¶12-13)
Kukhala olimba mwauzimu ndi komwe kungakuthandizeni kuthana ndi mavuto (Miy 24:16; w20.12 15)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 24:27—Kodi ndi mfundo iti imene tikupeza palembali? (w09 10/15 12)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 24:1-20 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Mwasiya kulankhula ndi munthu musanamulalikire. (lmd phunziro 2 mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 3 mfundo 4)
6. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Muuzeni kuti timaphunzira Baibulo ndi anthu ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za phunziro la Baibulo. (lmd phunziro 4 mfundo 3)
7. Nkhani
(3 min.) lmd zakumapeto A mfundo 11—Mutu: Mulungu Anatipatsa Uthenga Wofunika. (th phunziro 6)
Nyimbo Na. 99
8. Tizithandizana Tikakumana ndi Mavuto
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Miliri, ngozi zam’chilengedwe, zachiwawa, nkhondo kapena chizunzo zikhoza kuchitika mosayembekezereka. Zimenezi zikachitika, abale ndi alongo amene akhudzidwawo akhoza kuthandizana komanso kulimbikitsana. Komabe ngakhale kuti enafe sitinakhudzidwe mwachindunji, zimatiwawa ndipo timachita zonse zomwe tingathe kuti tiwathandize.—1Ak 12:25, 26.
Werengani 1 Mafumu 13:6 ndi Yakobo 5:16b. Kenako funsani funso ili:
N’chifukwa chiyani mapemphero amene atumiki a Yehova amapereka m’malo mwa anzawo amakhala amphamvu?
Werengani Maliko 12:42-44 ndi 2 Akorinto 8:1-4. Kenako funsani funso ili:
Ngakhale titakhala kuti sitipeza ndalama zambiri moti timangokwanitsa kupereka zochepa pa ntchito yapadziko lonse, n’chifukwa chiyani tiyenera kumaperekabe?
Onerani VIDIYO yakuti Kulimbikitsa Abale Ntchito Yathu Ikaletsedwa. Kenako funsani funso awa:
Kodi abale anasonyeza bwanji chikondi chololera kuvutikira ena pothandiza Akhristu anzawo amene anali m’madera omwe ntchito yathu inali yoletsedwa ku Eastern Europe?
Pa nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa, kodi abale anasonyeza bwanji kumvera lamulo lakuti azisonkhana komanso kulimbikitsana?—Ahe 10:24, 25
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 4-5