Lachitatu, October 22
Chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.—Yak. 2:17.
Yakobo ananena kuti munthu angamanene kuti ali ndi chikhulupiriro, koma zochita zake sizikusonyeza zimenezo. (Yak. 2:1-5, 9) Yakobo anafotokozanso za munthu yemwe anaona “m’bale kapena mlongo alibe zovala” koma sanamuthandize. Ngakhale munthu ameneyu atamanena kuti ali ndi chikhulupiriro, zingakhale zosamveka. (Yak. 2:14-16) Yakobo anatchula Rahabi monga chitsanzo cha munthu yemwe anasonyeza chikhulupiriro mwa zochita zake. (Yak. 2:25, 26) Iye anali atamva zokhudza Yehova ndiponso kuti ndi yemwe ankathandiza Aisiraeli. (Yos. 2:9-11) Rahabi anasonyeza chikhulupiriro mwa zochita zake poteteza Aisiraeli awiri omwe anabwera kudzafufuza dziko lawo ndipo moyo wawo unali pangozi. Izi zinachititsa kuti mayi wochimwayu, yemwenso sanali Mwisiraeli, aonedwe kuti ndi wolungama ngati mmene Abulahamu analili. Chitsanzo chake chimasonyeza kufunika kokhala ndi chikhulupiriro komanso ntchito zake. w23.12 5-6 ¶12-13
Lachinayi, October 23
Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko.—Aef. 3:17.
Monga Akhristu, sitimangokhutira ndi kumvetsa mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, timafunitsitsanso kudziwa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:9, 10) Bwanji osakonza zoti mufufuze mozama zinthu zomwe zingakuthandizeni kuti mukhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Mwachitsanzo, mungafufuze mmene anasonyezera kuti ankakonda atumiki ake akale komanso mmene zimenezo zimasonyezera kuti inunso amakukondani. Mungaphunzirenso zimene Yehova ankafuna kuti Aisiraeli azichita pomulambira n’kuziyerekezera ndi zimene amafuna kuti ifenso tizichita pomulambira masiku ano. Kapenanso mungaphunzire mozama zokhudza maulosi amene Yesu anakwaniritsa pa utumiki wake padziko lapansi. Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani lingakuthandizeni kuti muzisangalala pophunzira. Kuphunzira Baibulo mozama kungalimbitse chikhulupiriro chanu komanso kungakuthandizeni kuti ‘mumudziwedi Mulungu.’—Miy. 2:4, 5 w23.10 18-19 ¶3-5
Lachisanu, October 24
Koposa zonse, muzikondana kwambiri chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.—1 Pet. 4:8.
Mawu amene mtumwi Petulo anagwiritsa ntchito akuti “muzikondana kwambiri,” angatanthauze “kutambasula.” Mbali yachiwiri ya vesili ikufotokoza zotsatira za chikondi chimenechi. Ikuti chimakwirira machimo ochuluka a abale athu. Zili ngati timagwira chikondichi ndi manja awiri ngati mmene tingagwirire nsalu, n’kuchitambasula kuti chiphimbe, osati machimo ochepa, koma “machimo ochuluka.” Mawu akuti kuphimba, kapena kuti “kukwirira,” akufotokoza za kukhululuka. Mofanana ndi nsalu yomwe ingaphimbe malo akuda pa chovala, chikondi chimaphimba zimene abale athu amalakwitsa. Tiyenera kumakonda kwambiri abale athu moti tikhoza kuwakhululukira zolakwa zawo, ngakhale pamene kuchita zimenezi kungakhale kovuta. (Akol. 3:13) Tikakhululukira ena timasonyeza kuti timawakonda kwambiri komanso timafuna kusangalatsa Yehova. w23.11 11-12 ¶13-15