Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
126 Pamene Yehova anasonkhanitsa ndi kubwezeretsa ogwidwa ukapolo a Ziyoni,+
Tinakhala ngati tikulota.+
2 Pa nthawiyo tinaseka kwambiri,+
Ndipo lilime lathu linatulutsa mawu okondwa.+
Pamenepo anthu a mitundu ina anayamba kuuzana kuti:+
“Yehova wachitira anthu amenewa zinthu zazikulu.”+
3 Yehova watichitira zazikulu.+
Tasangalala.+
4 Sonkhanitsani ndi kubwezeretsa gulu lathu logwidwa ukapolo inu Yehova,+
Ngati mmene mumabwezeretsera madzi m’mitsinje ya ku Negebu.+
5 Amene akukhetsa misozi pofesa mbewu,+
Adzakolola akufuula mosangalala.+
6 Amene akupita kumunda akulira,+
Atasenza thumba lodzaza mbewu,+
Adzabwerako akufuula mosangalala,+
Atasenza mtolo wake wa zokolola.+