Masalimo
Salimo la Davide.
24 Dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi za Yehova,+
Nthaka ndi yake pamodzi ndi onse okhala panthakapo.+
4 Aliyense wopanda mlandu m’manja mwake ndi woyera mumtima mwake,+
Amene sanaone Moyo wanga ngati wopanda pake,+
Kapena kulumbira mwachinyengo.+
5 Ameneyo adzalandira madalitso kuchokera kwa Yehova,+
Adzalandira chilungamo kuchokera kwa Mulungu wa chipulumutso chake.+
6 Umenewo ndiwo m’badwo wa amene amafunafuna Mulungu,
M’badwo wa anthu ofunafuna nkhope yanu, inu Mulungu wa Yakobo.+ [Seʹlah.]
7 “Tukulani mitu yanu, inu zipata,+
Ndipo dzitukuleni, inu makomo akale lomwe,+
Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!”+
8 “Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndani?”+
“Ndi Yehova, wanyonga ndi wamphamvu,+
Yehova wamphamvu mu nkhondo.”+