Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Nehiloti.* Nyimbo ya Davide.
2 Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo,+
Inu Mfumu yanga+ ndi Mulungu wanga, chifukwa ndimapemphera kwa inu.+
4 Pakuti inu sindinu Mulungu wokondwera ndi zoipa,+
Palibe munthu woipa amene angakhale ndi inu ngakhale kwa kanthawi kochepa.+
5 Palibe anthu odzitama amene angaime pamaso panu.+
Mumadana ndi onse ochita zopweteka ena.+
6 Mudzawononga olankhula bodza.+
Munthu wokhetsa magazi+ ndi wachinyengo,+ Yehova amaipidwa naye.
7 Koma ine ndidzalowa m’nyumba yanu+
Chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha.+
Ndidzawerama nditayang’ana kumene kuli kachisi wanu wopatulika chifukwa chokuopani.+
8 Inu Yehova, nditsogolereni m’chilungamo chanu+ chifukwa adani anga andizungulira.+
Salazani njira yanu kuti ndiyendemo popanda chopunthwitsa.+
9 Pakuti m’kamwa mwawo simutuluka mawu okhulupirika.+
Mitima yawo yadzaza ndi zinthu zoipa.+
Mmero wawo ndi manda otseguka.+
Iwo amalankhula ndi lilime lachinyengo.+
10 Mulungu adzawapeza ndi mlandu.+
Adzagwa ndi ziwembu zawo zomwe.+
Muwamwaze chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zawo,+
Chifukwa iwo akupandukirani.+