Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Sauli anatumiza anthu, ndipo anali kudikirira nyumba yake kuti amuphe.+
2 Ndilanditseni kwa anthu ochita zopweteka anzawo,+
Ndipo ndipulumutseni kwa anthu amene ali ndi mlandu wa magazi.
3 Pakuti, taonani! Iwo akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+
Inu Yehova, anthu amphamvu akundiukira,+
Ngakhale kuti ine sindinapanduke kapena kuchita tchimo lililonse.+
4 Iwo akuthamanga ndi kukonzekera kundiukira, ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse.+
Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundichitikira.+
5 Inu Yehova, Mulungu wa makamu, ndinu Mulungu wa Isiraeli.+
Nyamukani ndi kuweruza mitundu yonse ya anthu.+
Musakomere mtima aliyense woipa ndi wachiwembu.+ [Seʹlah.]
7 Taonani! Amabwetuka ndi pakamwa pawo.+
Milomo yawo ili ngati malupanga,+
Pakuti iwo amati: “Ndani akumvetsera?”+
9 Inu Mphamvu yanga, ndidzayang’anabe kwa inu.+
Pakuti Mulungu ndiye malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+
10 Mulungu amene wandisonyeza kukoma mtima kosatha ndidzaonana naye maso ndi maso.+
Mulungu adzachititsa kuti ndione adani anga, adaniwo atagonja.+
11 Musawaphe, kuti anthu a mtundu wanga angaiwale.+
Ndi mphamvu zanu zochuluka achititseni kuyendayenda,+
Ndipo agwetseni, inu Yehova, chishango chathu,+
12 Chifukwa cha tchimo la pakamwa pawo, ndi mawu a pamilomo yawo.+
Agwidwe chifukwa cha kunyada kwawo,+
Chifukwa cha kutukwana ndi chinyengo zimene amachita mobwerezabwereza.
13 Afafanizeni mu mkwiyo wanu.+
Afafanizeni kuti asakhaleponso.
Ndipo adziwe kuti Mulungu akulamulira Yakobo mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi.+ [Seʹlah.]