Masalimo
Salimo lonena za Solomo.
72 Inu Mulungu, dziwitsani mfumu za zigamulo zanu,+
Ndipo dziwitsani mwana wa mfumu za chilungamo chanu.+
2 Aweruzire anthu milandu mwachilungamo,+
Ndipo aweruze milandu ya osautsika ndi ziweruzo zolungama.+
3 Mapiri atenge mtendere ndi kupita nawo kwa anthu,+
Komanso zitunda zitenge mtendere wopezeka mwachilungamo.
4 Aweruze osautsika pakati pa anthu,+
Apulumutse ana a anthu osauka,
Ndipo aphwanye wobera anzake mwachinyengo.
5 Iwo adzakuopani nthawi zonse pamene dzuwa likuwala,+
Adzakuopani ku mibadwomibadwo pamene mwezi uli kuthambo.+
6 Adzatsika ngati mvula pa udzu umene wadulidwa,+
Ngati mvula yambiri yamvumbi imene imanyowetsa kwambiri nthaka.+
7 M’masiku ake, wolungama adzaphuka,+
Ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.+
8 Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja,+
Komanso kuchokera ku Mtsinje*+ kukafika kumalekezero a dziko lapansi.+
10 Mafumu a ku Tarisi ndi m’zilumba+
Adzapereka msonkho.+
Mafumu a ku Sheba ndi Seba
Adzapereka mphatso.+
12 Pakuti adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo,+
Komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza.+
14 Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa,
Ndipo adzaona magazi awo kukhala amtengo wapatali.+
15 Iye akhale ndi moyo wautali,+ ndipo apatsidwe wina mwa golide wa ku Sheba.+
Nthawi zonse anthu azimupempherera.
Adalitsike tsiku lililonse.+
16 Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.+
Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.+
Zokolola za mfumu zidzachuluka ngati mitengo ya ku Lebanoni,+
Ndipo anthu ochokera mumzinda adzaphuka ngati udzu wa panthaka.+
17 Dzina lake likhalebe mpaka kalekale.+
Nthawi zonse pamene dzuwa latuluka, dzina lake lizitchuka,
Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.*+
Mitundu yonse ya anthu imutche wodala.+