Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Mutilabeni.* Nyimbo ya Davide.
א [ʼAʹleph]
2 Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha inu,+
Ndidzaimba nyimbo motsagana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+
ב [Behth]
4 Chifukwa mwandiweruzira mlandu wanga ndi dandaulo langa.+
Mwakhala pampando wachifumu ndipo mukuweruza mwachilungamo.+
ג [Giʹmel]
5 Mwadzudzula anthu a mitundu ina,+ mwawononga oipa.+
Dzina lawo mwalifafaniza mpaka kalekale, mwalifafaniza mpaka muyaya.+
6 Kusakaza kwa mdani kwatheratu tsopano,+
Mizinda imene mwaifafaniza, nayonso yatheratu.+
Dzina la mdani wanu silidzatchulidwanso.+
ה [Heʼ]
7 Koma Yehova adzakhala pampando wachifumu mpaka kalekale,+
Adzakhazikitsa mpando wake wachifumu kuti aweruze.+
8 Iye adzaweruza anthu padziko lapansi mwachilungamo.+
Adzazenga mlandu mitundu ya anthu moyenerera.+
ו [Waw]
9 Yehova adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo kwa aliyense woponderezedwa,+
Adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo m’nthawi za masautso.+
10 Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani,+
Pakuti simudzasiya ndithu anthu okufunafunani, inu Yehova.+
ז [Zaʹyin]
11 Anthu inu, imbani nyimbo motsagana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda Yehova amene akukhala m’Ziyoni.+
Fotokozani ntchito zake kwa mitundu ya anthu.+
12 Pofunafuna okhetsa magazi,+ iye adzakumbukira ndithu anthu osautsidwa.+
Sadzaiwala ndithu kulira kwawo.+
ח [Chehth]
13 Ndikomereni mtima inu Yehova. Onani mmene anthu odana nane akundisautsira,+
Inu Mulungu amene mukundinyamula kundichotsa pazipata za imfa.+
14 Ndichitireni zimenezi kuti ndilengeze ntchito zanu zonse zotamandika+
Pazipata+ za mwana wamkazi wa Ziyoni,+
Kuti ndikondwere ndi chipulumutso chanu.+
ט [Tehth]
16 Yehova amadziwika ndi ziweruzo zimene amapereka.+
Woipa wakodwa mumsampha wa ntchito ya manja ake.+
Higayoni.* [Seʹlah.]
י [Yohdh]
18 Pakuti waumphawi sadzaiwalidwa nthawi zonse,+
Ndiponso chiyembekezo cha ofatsa sichidzatha konse.+
כ [Kaph]