22 tiyeni timufikire Mulungu ndi mitima yoona. Tichite zimenezi tilibe chikayikiro chilichonse komanso tili ndi chikhulupiriro, pakuti mitima yathu yayeretsedwa kuti isakhalenso ndi chikumbumtima choipa,+ ndipo matupi athu asambitsidwa m’madzi oyera.+