Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 18:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Motero iwo anali kuweruza anthuwo pa nkhani iliyonse yoyenera. Nkhani yovuta anali kupita nayo kwa Mose,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza anali kuisamalira.

  • Deuteronomo 16:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mudziikire oweruza+ ndi atsogoleri+ m’mizinda yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, malinga ndi mafuko anu. Oweruza ndi atsogoleriwo aziweruza anthu ndi chiweruzo cholungama.

  • Deuteronomo 17:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Mlandu wofuna chigamulo ukakukulira kwambiri,+ monga mlandu wokhudza kukhetsa magazi,+ mlandu umene munthu wakasuma,+ mlandu wokhudza zachiwawa kapena mkangano+ umene wachitika mumzinda wanu, pamenepo uzinyamuka ndi kupita kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+

  • Deuteronomo 22:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndiyeno akulu+ a mzindawo azigwira mwamunayo ndi kum’langa.+

  • 2 Mbiri 19:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene akukhala m’mizinda yawo, wokhudza kukhetsa magazi,+ chilamulo,+ ndi zigamulo,+ muziwachenjeza kuti asalakwire Yehova kuopera kuti mkwiyo wa Mulungu+ ungakuyakireni inuyo ndi abale anu. Muzichita zimenezi n’cholinga choti musapalamule mlandu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena