Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 7:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Nganga ya nsembe yoweyula+ ndiponso mwendo, umene ndi gawo lopatulika, ndikuzitenga pansembe zachiyanjano za ana a Isiraeli. Ndikuzitenga kwa ana a Isiraeli ndi kuzipereka kwa Aroni wansembe ndi ana ake. Ili ndi lamulo mpaka kalekale.

  • Levitiko 10:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Mudyenso nganga ya nsembe yoweyula,*+ ndi mwendo umene ndi gawo lopatulika.+ Muzidyere m’malo oyera, inuyo, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ Muyenera kutero chifukwa zapatsidwa kwa inu monga gawo lanu ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zachiyanjano za ana a Isiraeli.

  • Numeri 18:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Gawo limenelo lizikhala lako pazopereka zopatulika koposa, ndizo nsembe zonse zotentha ndi moto. Nsembezo, zimene azibwera nazo kwa ine, ndi izi: Nsembe zawo zambewu,+ nsembe zawo zamachimo,+ nsembe zawo za kupalamula,+ ndi nsembe zawo zina zonse. Gawolo lizikhala chinthu chopatulika koposa kwa iwe ndi ana ako.

  • Deuteronomo 18:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Uziperekanso gawo loyamba la mbewu zako, vinyo wako watsopano, mafuta ndi ubweya wa nkhosa wometedwa moyambirira.+

  • 1 Akorinto 9:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Kodi simukudziwa kuti anthu ochita ntchito zopatulika amadya+ za m’kachisi, ndipo amene amatumikira+ kuguwa lansembe nthawi zonse amagawana gawo ndi guwa lansembe?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena