Levitiko 4:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 ng’ombe yonseyo aziitenga ndi kupita nayo kunja kwa msasa.+ Azipita nayo kumalo oyera kumene amataya phulusa losakanizika ndi mafuta+ ndipo aziitentha pamoto wa nkhuni.+ Azitentha ng’ombeyo kumalo otayako phulusa losakanizika ndi mafuta. Levitiko 16:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 “Koma ng’ombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndi mbuzi ya nsembe yamachimo zimene magazi ake analowa nawo m’malo oyera pokaphimba machimo, azizitulutsira kunja kwa msasa ndipo azitentha pamoto zikopa zake, nyama ndi ndowe zake.+ Numeri 19:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “‘Ndiyeno munthu wosadetsedwa awole phulusa+ la ng’ombeyo, akalithire pamalo oyera kunja kwa msasawo. Phulusalo alisunge kuti azilithira m’madzi oyeretsera+ khamu la ana a Isiraeli. Imeneyi ndi nsembe yamachimo. Aheberi 13:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Zinalinso chimodzimodzi ndi Yesu. Kuti ayeretse+ anthu ndi magazi ake,+ anakavutikira kunja kwa chipata.+
12 ng’ombe yonseyo aziitenga ndi kupita nayo kunja kwa msasa.+ Azipita nayo kumalo oyera kumene amataya phulusa losakanizika ndi mafuta+ ndipo aziitentha pamoto wa nkhuni.+ Azitentha ng’ombeyo kumalo otayako phulusa losakanizika ndi mafuta.
27 “Koma ng’ombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndi mbuzi ya nsembe yamachimo zimene magazi ake analowa nawo m’malo oyera pokaphimba machimo, azizitulutsira kunja kwa msasa ndipo azitentha pamoto zikopa zake, nyama ndi ndowe zake.+
9 “‘Ndiyeno munthu wosadetsedwa awole phulusa+ la ng’ombeyo, akalithire pamalo oyera kunja kwa msasawo. Phulusalo alisunge kuti azilithira m’madzi oyeretsera+ khamu la ana a Isiraeli. Imeneyi ndi nsembe yamachimo.
12 Zinalinso chimodzimodzi ndi Yesu. Kuti ayeretse+ anthu ndi magazi ake,+ anakavutikira kunja kwa chipata.+