-
Levitiko 12:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Ndiyeno masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaing’ono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa+ kuti ikhale nsembe yamachimo.
-