-
Levitiko 11:32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 “‘Tsopano chamoyo chilichonse mwa zimenezi chikafa n’kugwera pa chinthu china chilichonse, chinthucho chizikhala chodetsedwa. Kaya ndi chiwiya chamtengo,+ chovala, chikopa,+ kapena chiguduli*+ chizikhala chodetsedwa. Chiwiya chilichonse chimene chimagwiritsidwa ntchito chiziikidwa m’madzi, koma chizikhala chodetsedwa kufikira madzulo, kenako chizikhala choyera.
-