33 Pamenepo Mose anagawira malo ana a Gadi+ ndi ana a Rubeni.+ Anagawiranso malo hafu ya fuko la Manase+ mwana wa Yosefe. Anawagawira malo a ufumu wa Sihoni+ mfumu ya Aamori, ndi a ufumu wa Ogi+ mfumu ya Basana, dera lonse la mizinda ndi midzi yozungulira.
12Tsopano awa ndi mafumu amene ana a Isiraeli anagonjetsa n’kulanda madera awo, kumbali yotulukira dzuwa+ ya mtsinje wa Yorodano. Analanda kuchokera kuchigwa* cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba+ konse, kumbali yotulukira dzuwa. Mafumu ake ndi awa:
33 Anayambira ku Yorodano chakotulukira dzuwa, dziko lonse la Giliyadi,+ Agadi,+ Arubeni+ ndi Amanase,+ kuyambira ku Aroweli+ yemwe ali pafupi ndi chigwa* cha Arinoni, ngakhalenso Giliyadi ndi Basana.+