33 Pamenepo Mose anagawira malo ana a Gadi+ ndi ana a Rubeni.+ Anagawiranso malo hafu ya fuko la Manase+ mwana wa Yosefe. Anawagawira malo a ufumu wa Sihoni+ mfumu ya Aamori, ndi a ufumu wa Ogi+ mfumu ya Basana, dera lonse la mizinda ndi midzi yozungulira.
12 Choncho pa nthawi imeneyo tinatenga dzikoli kukhala lathu. Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa Aroweli,+ mzinda umene uli m’chigwa cha Arinoni, ndi hafu ya dera lamapiri la Giliyadi, ndi mizinda yake.
13 Hafu ya fuko la Manase ndinalipatsa dera lotsala la Giliyadi+ ndi Basana+ yense wa ufumu wa Ogi. Kodi si paja dera lonse la Arigobi+ limene ndi Basana yense, limatchedwa dziko la Arefai?+