5 dziko la Agebala+ ndiponso dziko lonse la Lebanoni, kotulukira dzuwa, kuyambira ku Baala-gadi+ m’munsi mwa phiri la Herimoni mpaka kumalire ndi Hamati.+
2 Pitani mukaone ku Kaline ndipo kuchokera kumeneko mukapite ku Hamati+ kumene kuli anthu ambiri, kenako mukapite ku Gati+ wa Afilisiti. Kodi mizinda imeneyi imaposa maufumu anu awiriwa?* Kapena kodi malo awo ndi aakulu kuposa malo anu?+