Ekisodo 17:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Ndiyeno anthu anayamba kukangana ndi Mose kuti:+ “Tipatse madzi timwe.” Koma Mose anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyesa Yehova?”+ Salimo 95:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pamene makolo anu anandiyesa.+Iwo anandisanthula, ndipo anaonanso ntchito zanga.+ Salimo 106:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Anasonyeza chikhumbo chawo chadyera m’chipululu,+Ndipo anayesa Mulungu m’chipululumo.+ Aheberi 3:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Kodi paja ndi ndani amene anamva koma n’kupsetsa mtima Mulungu?+ Kodi si anthu onse amene anatuluka m’dziko la Iguputo motsogoleredwa ndi Mose?+
2 Ndiyeno anthu anayamba kukangana ndi Mose kuti:+ “Tipatse madzi timwe.” Koma Mose anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyesa Yehova?”+
16 Kodi paja ndi ndani amene anamva koma n’kupsetsa mtima Mulungu?+ Kodi si anthu onse amene anatuluka m’dziko la Iguputo motsogoleredwa ndi Mose?+