41 “Pamenepo munayankha ndi kundiuza kuti, ‘Tachimwira Yehova.+ Ife tipitadi kukamenya nkhondo mogwirizana ndi zonse zimene Yehova Mulungu wathu watilamula!’ Choncho aliyense wa inu anamanga m’chiuno zida zake zankhondo, ndipo munaona ngati n’zosavuta kukwera m’phirimo.+