Amosi 3:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonse asanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.+ Mateyu 11:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate+ okha, komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha+ ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.+ Aefeso 3:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 M’mibadwo ina, chinsinsi+ chimenechi sichinaululidwe kwa ana a anthu mmene chaululidwira+ tsopano kwa atumwi ndi aneneri+ ake oyera mwa mzimu.
7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonse asanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.+
27 Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate+ okha, komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha+ ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.+
5 M’mibadwo ina, chinsinsi+ chimenechi sichinaululidwe kwa ana a anthu mmene chaululidwira+ tsopano kwa atumwi ndi aneneri+ ake oyera mwa mzimu.