12 Pambuyo pake Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Chifukwa simunasonyeze chikhulupiriro mwa ine, polephera kundilemekeza+ pamaso pa ana a Isiraeli, simudzaulowetsa mpingowu m’dziko limene ndidzawapatse.”+
27 Kwera pamwamba pa Pisiga+ ndi kukweza maso ako, ndipo uyang’ane kumadzulo, kumpoto, kum’mwera ndi kum’mawa, uone dzikolo ndi maso ako, chifukwa suwoloka Yorodano uyu.+