Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 18:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “‘Usalole kuti aliyense mwa ana ako aperekedwe+ kwa Moleki.*+ Usanyoze+ dzina la Mulungu wako mwa njira imeneyi. Ine ndine Yehova.+

  • Deuteronomo 12:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Usapembedze Yehova Mulungu wako m’njira imeneyi,+ pakuti iwo amachitira milungu yawo zonse zimene zili zonyansa kwa Yehova, zimene iye amadana nazo. Pakuti iwo nthawi zonse amatentha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto monga nsembe kwa milungu yawo.+

  • 2 Mafumu 16:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Anayenda m’njira ya mafumu a ku Isiraeli,+ ndipo ngakhale mwana wake wamwamuna anamuwotcha* pamoto,+ mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa chifukwa cha ana a Isiraeli.

  • 2 Mbiri 28:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ahazi anafukiza nsembe yautsi+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Iye anawotcha ana ake+ pamoto mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+

  • Salimo 106:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Anali kupereka nsembe ana awo aamuna+

      Ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.+

  • Yeremiya 19:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Iwo amangiranso Baala malo okwezeka kuti azitentherapo ana awo aamuna monga nsembe zopsereza zathunthu zoperekedwa kwa Baala.+ Ine sindinawalamule zimenezi kapena kuzitchula,+ ndipo sindinaziganizirepo mumtima mwanga.”’+

  • Yeremiya 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kuwonjezera apo anamangira Baala+ malo okwezeka m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Anachita izi kuti azidutsitsa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto monga nsembe+ kwa Moleki.+ Ine sindinawalamule zimenezi+ ndipo sindinaganizirepo mumtima mwanga kuchita chinthu chonyansa chimenechi,+ kuti Yuda achite tchimo.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena