2 Muyenera kuphunzira zimenezi kuti muziopa+ Yehova Mulungu wanu, n’cholinga choti masiku onse a moyo wanu muzisunga mfundo zake ndi malamulo ake amene ndikukuuzani, inuyo, ana anu ndi zidzukulu zanu,+ ndiponso kuti masiku anu atalike.+
7 Kodi ndani amene sangakuopeni,+ inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa, chifukwa chakuti pakati pa anzeru onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+