7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya m’dera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, m’dera lamapiri la Yuda.
5 Iye anali kukhala patsinde pa mtengo wa kanjedza wa Debora, pakati pa mzinda wa Rama+ ndi wa Beteli,+ m’dera lamapiri la Efuraimu. Ana a Isiraeli anali kupita kwa iye kukalandira zigamulo zochokera kwa Mulungu.