Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 20:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, musachite nawo mantha mukaona kuti ali ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo,+ ndiponso mukaona kuti adani anuwo ndi ochuluka kwambiri kuposa inu. Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ali ndi inu.+

  • Deuteronomo 31:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Limbani mtima ndipo chitani zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.”+

  • Yoswa 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ine ndidzapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli anthu onse okhala kudera lamapiri, kuchokera ku Lebanoni+ mpaka ku Misirepotu-maimu,+ ndidzapitikitsa Asidoni onse.+ Iweyo ungopereka dzikoli kwa ana a Isiraeli+ kuti likhale cholowa chawo monga mmene ndinakulamulira.+

  • Salimo 27:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+

      Ndingaopenso ndani?+

      Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+

      Ndingachitenso mantha ndi ndani?+

  • Aroma 8:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+

  • Aheberi 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Moti tikhale olimba mtima ndithu+ ndipo tinene kuti: “Yehova* ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena