8 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Aisiraeli,+ moti anawagulitsa+ kwa Kusani-risataimu, mfumu ya Mesopotamiya.+ Ana a Isiraeli anatumikira Kusani-risataimu zaka 8.
16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.