Levitiko 26:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Ndidzabweretsa lupanga pa inu lobwezera chilango+ chifukwa cha pangano.+ Pamenepo mudzathawira m’mizinda yanu, ndipo ndidzakutumizirani mliri pakati panu+ ndi kukuperekani m’manja mwa mdani.+ Deuteronomo 28:48 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 48 Udzatumikira adani ako+ amene Yehova adzawatuma kuti akuukire. Udzawatumikira uli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso ukusowa china chilichonse. Adzakuveka goli lachitsulo m’khosi lako kufikira atakufafaniza.+
25 Ndidzabweretsa lupanga pa inu lobwezera chilango+ chifukwa cha pangano.+ Pamenepo mudzathawira m’mizinda yanu, ndipo ndidzakutumizirani mliri pakati panu+ ndi kukuperekani m’manja mwa mdani.+
48 Udzatumikira adani ako+ amene Yehova adzawatuma kuti akuukire. Udzawatumikira uli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso ukusowa china chilichonse. Adzakuveka goli lachitsulo m’khosi lako kufikira atakufafaniza.+