32 M’kupita kwa nthawi, Gidiyoni mwana wa Yowasi anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino ndi wautali, ndipo anamuika m’manda a Yowasi bambo ake, mumzinda wa Ofira wa Aabi-ezeri.+
5 Atatero anapita kunyumba ya bambo ake ku Ofira+ ndi kupha abale ake,+ ana aamuna 70 a Yerubaala, pamwala umodzi. Koma sanaphe Yotamu, mwana wamng’ono kwambiri mwa ana aamuna a Yerubaala, chifukwa anali atabisala.