Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 23:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Chifukwa chake n’chakuti, sanakuthandizeni+ ndi mkate ndi madzi pamene munali pa ulendo mutatuluka mu Iguputo,+ ndiponso chifukwa chakuti analemba ganyu Balamu mwana wa Beori, amene kwawo ndi ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.+

  • Oweruza 5:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Mngelo wa Yehova+ anati: ‘Tembererani+ Merozi,

      Tembererani anthu ake mosaleka,

      Chifukwa sanathandize Yehova,

      Sanabwere ndi anthu amphamvu kudzathandiza Yehova.’

  • 1 Samueli 25:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pamenepo Nabala anayankha atumiki a Davide kuti: “Kodi Davide ndani,+ ndipo mwana wa Jese ndani? Masiku ano atumiki amene akuthawa ambuye awo achuluka kwabasi.+

  • 1 Samueli 25:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndiye ine nditenge mkate wanga,+ madzi ndi nyama imene ndaphera anyamata anga ometa ubweya wa nkhosa n’kupereka kwa amuna amene sindikudziwa m’pang’ono pomwe kumene achokera?”+

  • Miyambo 3:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo,+ pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.+

  • Yakobo 2:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 koma wina mwa inu n’kunena kuti: “Yendani bwino, mupeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,” koma osamupatsa zimene thupi lake likusowazo, kodi pali phindu lanji?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena