24 Malo alionse amene mapazi anu adzapondapo adzakhala anu.+ Malire a dziko lanu adzayambira kuchipululu kukafika ku Lebanoni, kuyambira ku mtsinje wa Firate, kukafika kunyanja ya kumadzulo.+
4 Dziko lanu lidzayambira kuchipululu ndi ku Lebanoni uyu mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate, dziko lonse la Ahiti+ mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu, kolowera dzuwa.+