12 Choncho pa nthawi imeneyo tinatenga dzikoli kukhala lathu. Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa Aroweli,+ mzinda umene uli m’chigwa cha Arinoni, ndi hafu ya dera lamapiri la Giliyadi, ndi mizinda yake.
13 Hafu ya fuko la Manase ndinalipatsa dera lotsala la Giliyadi+ ndi Basana+ yense wa ufumu wa Ogi. Kodi si paja dera lonse la Arigobi+ limene ndi Basana yense, limatchedwa dziko la Arefai?+