7Chotero amuna a ku Kiriyati-yearimu+ anabweradi ndi kutenga likasa la Yehova n’kupita nalo kwawo, ndipo analiika m’nyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Anapatula Eleazara mwana wake kuti azilondera likasa la Yehova.
4 Koma Davide anali atachotsa likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu+ n’kukaliika kumalo amene iye anakonza,+ pakuti anali atamanga hema wa likasalo ku Yerusalemu.+