1 Samueli 24:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Tsopano ngati munthu wapeza mdani wake, kodi angamulole kupita mwamtendere?+ Chonchotu Yehova adzakufupa ndi zinthu zabwino,+ chifukwa chakuti lero wandichitira zabwino. Yobu 34:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake. Miyambo 28:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+ Aheberi 6:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pakuti Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake,+ mwa kutumikira oyera+ ndipo mukupitiriza kuwatumikira.
19 Tsopano ngati munthu wapeza mdani wake, kodi angamulole kupita mwamtendere?+ Chonchotu Yehova adzakufupa ndi zinthu zabwino,+ chifukwa chakuti lero wandichitira zabwino.
11 Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake.
20 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+
10 Pakuti Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake,+ mwa kutumikira oyera+ ndipo mukupitiriza kuwatumikira.