7 Iyeyu atafika anapempha kuti, ‘Chonde ndikunkheko.+ Ndizitola balere wotsala m’mbuyo mwa okololawo.’ Atatero, analowa m’mundamu n’kuyamba kukunkha. Wakhala akukunkha kuyambira m’mawa mpaka posachedwapa pamene anakhala pansi pang’ono m’chisimbamu.”+