2 Nthawi ina anauza mayi ake kuti: “Ndalama zanu zasiliva zokwana 1,100 zimene zinasowa zija, zimene munatemberera+ nazo munthu amene anazibayo, ine ndikumva, zili ndi ine. Ndine amene ndinatenga.”+ Pamenepo mayi akewo anati: “Yehova akudalitse mwana wanga.”+