Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 14:50
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 50 Mkazi wa Sauli dzina lake anali Ahinowamu, mwana wamkazi wa Ahimazi. Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Abineri+ mwana wa Nera, m’bale wa bambo ake a Sauli.

  • 1 Samueli 17:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisiti uja, anafunsa Abineri,+ mkulu wa asilikali, kuti: “Kodi ameneyu ndi mwana+ wa ndani,+ Abineri?” Poyankha Abineri anati: “Ndikulumbira pali moyo wanu mfumu, ine sindikudziwa ngakhale pang’ono!”

  • 2 Samueli 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndiyeno Abineri+ mwana wa Nera, amene anali mtsogoleri wa asilikali a Sauli, anatenga Isi-boseti+ mwana wa Sauli ndi kuwolokera naye ku Mahanaimu.+

  • 2 Samueli 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Abineri atamva mawu amenewa a Isi-boseti anakwiya kwambiri+ n’kunena kuti: “Kodi ine ndine galu+ wopanda pake wa Yuda? Ineyo ndikusonyeza kukoma mtima kosatha ku nyumba ya Sauli bambo ako, abale ake ndi mabwenzi ake apamtima, ndipo ndikukuteteza kuti usagwe m’manja mwa Davide, koma lero ukundiimba mlandu wa cholakwa chokhudza mkazi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena