25 Chonde mbuyanga, musaganizire za Nabala, munthu wopanda pakeyu,+ chifukwa zochita zake ndi zogwirizana ndi dzina lake. Dzina lake ndi Nabala ndipo ndi wopandadi nzeru.+ Koma ine kapolo wanu wamkazi sindinawaone anyamata amene inu mbuyanga munawatuma.