27 Pamenepo mfumu inapitiriza kuuza Zadoki wansembe kuti: “Iwe ndi wamasomphenya,*+ si choncho kodi? Bwerera kumzinda mu mtendere. Bwerera pamodzi ndi Ahimazi mwana wako wamwamuna ndi Yonatani+ mwana wamwamuna wa Abiyatara. Mubwerere ndi ana anu awiri amene muli nawowa.
29 Nkhani zokhudza Davide mfumu, zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa pakati pa mawu a Samueli wamasomphenya,*+ Natani+ mneneri, ndiponso pakati pa mawu a Gadi+ wamasomphenya.